-
Oweruza 3:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Aisiraeli atafuulira Yehova kuti awathandize,+ Yehova anawapatsa munthu woti awapulumutse.+ Munthu wake anali Otiniyeli,+ mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. 10 Mzimu wa Yehova unkamuthandiza+ ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Mesopotamiya* mʼmanja mwake, moti anamugonjetsa. 11 Zitatero dziko linakhala pa mtendere zaka 40. Kenako Otiniyeli, mwana wa Kenazi, anamwalira.
-