-
Numeri 35:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Koma ngati wamukankha mwangozi, osati chifukwa choti amadana naye, kapena ngati wamugenda ndi chinachake mwangozi, osati ndi zolinga zoipa,*+ 23 kapena ngati samamuona ndipo wamugwetsera mwala, mnzakeyo nʼkufa, koma sanali mdani wake komanso analibe cholinga choti amuvulaze, 24 oweruza aweruze pakati pa wopha mnzakeyo ndi woyenera kubwezera magaziyo, mogwirizana ndi malamulo amenewa.+
-
-
Deuteronomo 19:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiye zimene zizichitika ndi munthu amene wapha mnzake nʼkuthawira kumeneko kuti akhale ndi moyo ndi izi: Ngati wapha mnzake mwangozi ndipo sankadana naye,+ 5 mwachitsanzo, munthu akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake nʼkumenya mnzakeyo mpaka kumupha, amene wapha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 6 Akapanda kutero, chifukwa chakuti wobwezera magazi+ ndi wokwiya kwambiri,* angathamangitse wopha munthuyo nʼkumupeza kenako nʼkumumpha chifukwa chakuti mtunda wopita kumzindawo unali wautali. Koma wopha mnzake mwangoziyo samayenera kufa chifukwa sankadana ndi mnzakeyo.+
-