-
Yoswa 2:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ndipo anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani dzikoli+ ndipo tonse tikuchita nanu mantha.+ Aliyense mʼdzikoli mtima wake suli mʼmalo chifukwa cha inu.+ 10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano. 11 Titangomva zimenezi tinataya mtima,* ndipo chifukwa cha inu, palibe aliyense amene akulimba mtima. Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi.+
-