-
Genesis 17:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mulungu anapitiriza kuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbadwa zako mʼmibadwo yawo yonse. 10 Ili ndi pangano la pakati pa ine ndi iwe, lakuti iwe ndi mbadwa zako muzilisunga: Mwamuna aliyense pakati panu azidulidwa.+ 11 Muzichita mdulidwe* kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+
-