5 Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti kuti: “Agawireni mkate anthu amene akunditsatirawa chifukwa atopa. Ndikuthamangitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.” 6 Koma akalonga a ku Sukoti anayankha kuti: “Tipatse asilikali ako mkate chifukwa chiyani? Wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?”