9 Choncho Esau anapita kwa Isimaeli* nʼkukatengako mkazi wina kuwonjezera pa akazi amene anali nawo. Mkaziyo dzina lake anali Mahalati ndipo anali mchemwali wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu.+
28 Pamene amalonda a Chimidiyani+ aja ankadutsa, abale a Yosefe anamutulutsa mʼchitsimemo nʼkumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo amalondawo anapita naye ku Iguputo.