-
Yoswa 21:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mabanja a ana a Kohati, kapena kuti Alevi otsala, anapatsidwa mizinda yochokera mʼfuko la Efuraimu pambuyo pochita maere. 21 Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto mʼdera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto,
-