-
Oweruza 3:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kenako anawauza kuti: “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka adani anu Amowabu mʼmanja mwanu.” Atatero, anamʼtsatira kukatsekereza Amowabu pamalo owolokera mtsinje wa Yorodano, ndipo sanalole aliyense kuwoloka.
-
-
Oweruza 7:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Gidiyoni anatumiza uthenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu, wakuti: “Pitani ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna mʼmalo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ingʼonoingʼono mpaka ku Beti-bara.
-