-
Yoswa 19:47, 48Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Koma fuko la Dani gawo lawo linkawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo nʼkupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga nʼkuyamba kukhalamo ndipo anausintha dzina loti Lesemu nʼkuupatsa dzina loti Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ 48 Ichi chinali cholowa cha fuko la Dani motsatira mabanja awo, ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
-