-
Oweruza 17:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mika atabweza ndalamazo kwa mayi ake, mayi akewo anatenga ndalama zasiliva 200 nʼkuzipereka kwa wosula siliva. Wosula silivayo anapanga zifaniziro ziwiri. Zifanizirozi anaziika mʼnyumba ya Mika. 5 Mika anali ndi nyumba ya milungu ndipo anapanga efodi+ ndi aterafi,*+ komanso anapatsa mmodzi mwa ana ake udindo woti akhale wansembe wake.+
-