Levitiko 5:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kapenanso munthu akafulumira kulumbira kuti achita chinachake, kaya chabwino kapena choipa koma sanazindikire, kenako nʼkuzindikira kuti analumbira mofulumira, ndiye kuti wapalamula mlandu.*+ Levitiko 19:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Musamalumbire zabodza mʼdzina langa+ nʼkuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. Mateyu 5:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musamalumbire koma osachita,+ mʼmalomwake muzikwaniritsa zimene mwalonjeza kwa Yehova.’*+
4 Kapenanso munthu akafulumira kulumbira kuti achita chinachake, kaya chabwino kapena choipa koma sanazindikire, kenako nʼkuzindikira kuti analumbira mofulumira, ndiye kuti wapalamula mlandu.*+
33 Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musamalumbire koma osachita,+ mʼmalomwake muzikwaniritsa zimene mwalonjeza kwa Yehova.’*+