Ekisodo 24:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu nʼkuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Atatero anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+ Ekisodo 24:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Choncho Mose anatenga magaziwo nʼkuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapangana nanu mogwirizana ndi mawu onsewa.”+ Ekisodo 34:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ulembe mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+ Deuteronomo 29:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Awa ndi mawu a pangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisiraeli mʼdziko la Mowabu, kuwonjezera pa pangano limene anachita nawo ku Horebe.+ Yoswa 23:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Mukadzaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, Yehova adzakukwiyirani kwambiri+ ndipo simudzachedwa kutha padziko labwino limene iye anakupatsani.”+
3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu nʼkuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Atatero anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+
8 Choncho Mose anatenga magaziwo nʼkuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapangana nanu mogwirizana ndi mawu onsewa.”+
27 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ulembe mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+
29 Awa ndi mawu a pangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisiraeli mʼdziko la Mowabu, kuwonjezera pa pangano limene anachita nawo ku Horebe.+
16 Mukadzaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, Yehova adzakukwiyirani kwambiri+ ndipo simudzachedwa kutha padziko labwino limene iye anakupatsani.”+