13 Tsopano Yoswa anali atakalamba, ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Choncho Yehova anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba ndipo uli ndi zaka zambiri, koma madera oti alandidwe adakali ambiri. 2 Madera amene atsala ndi awa:+ Madera onse a Afilisiti ndi madera onse a Agesuri.+