-
1 Samueli 6:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Iwo anayankha kuti: “Ngati mukubweza likasa lapangano la Yehova Mulungu wa Isiraeli, musalibweze popanda kupereka nsembe. Mulimonse mmene zingakhalire, muyenera kupereka nsembe yakupalamula.+ Mukatero mudzachira ndipo mudzadziwa chifukwa chake dzanja lake silinasiye kukukhaulitsani.” 4 Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe yakupalamula imene tiyenera kumutumizira ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi olosera aja anati: “Mutumize zifaniziro 5 zagolide za matenda a mudzi, ndi zifaniziro 5 zagolide za mbewa, mogwirizana ndi chiwerengero cha olamulira a Afilisiti.+ Muchite zimenezi chifukwa mliriwu wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu.
-