-
2 Samueli 1:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno Davide anafunsa mnyamata amene anabweretsa uthengawo kuti: “Kodi kwanu nʼkuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wa Mwamaleki, amene anabwera kudzakhala ndi Aisiraeli.” 14 Davide anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani sunaope kupha wodzozedwa wa Yehova?”+ 15 Atatero, Davide anaitana mmodzi mwa anyamata ake nʼkumuuza kuti: “Bwera kuno udzamuphe.” Choncho iye anamuphadi.+
-