-
Deuteronomo 23:3-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mbadwa ya Amoni kapena Mowabu isamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zawo zisadzalowe mumpingo wa Yehova mpaka kalekale, 4 chifukwa chakuti sanakuthandizeni pokupatsani chakudya ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ komanso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+ 5 Koma Yehova Mulungu wanu anakana kumvera Balamu.+ Mʼmalomwake, Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ 6 Musamachite chilichonse powathandiza kuti azikhala mwamtendere komanso kuti zinthu ziwayendere bwino masiku onse a moyo wanu.+
-