-
1 Mbiri 18:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Toi, mfumu ya Hamati, atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba,+ 10 nthawi yomweyo anatumiza mwana wake Hadoramu kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndiponso kukamuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri nʼkumugonjetsa. (Chifukwa Hadadezeri ankakonda kumenyana ndi Toi.) Popita kwa Davide, Hadoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zakopa. 11 Mfumu Davide anapereka zinthu zimenezi kwa Yehova+ pamodzi ndi siliva komanso golide amene anatenga kuchokera ku mitundu yonse. Anatenga kuchokera kwa Aedomu, Amowabu, Aamoni,+ Afilisiti+ ndi Aamaleki.+
-