27 Mfumu inauza Zadoki wansembe kuti: “Paja iwe ndiwe wamasomphenya.+ Iwe ndi Abiyatara bwererani kumzinda mwamtendere. Mubwerere pamodzi ndi ana anu awiri, Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara.
3 Davide, komanso Zadoki+ yemwe anali wochokera mwa ana a Eleazara, ndiponso Ahimeleki wochokera mwa ana a Itamara, anagawa ana a Aroniwo mʼmagulu mogwirizana ndi udindo wa utumiki wawo.