-
2 Samueli 19:41, 42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Kenako anthu ena a ku Isiraeli anabwera kwa mfumu nʼkunena kuti: “Nʼchifukwa chiyani abale athu a ku Yuda akubweretsani mozemba inu mfumu, pamodzi ndi banja lanu komanso anthu onse amene munali nawo kutsidya la Yorodano?”+ 42 Anthu a ku Yuda anayankha anthu a ku Isiraeli kuti: “Chifukwa chakuti mfumuyi ndi wachibale wathu.+ Ndiye inu mwakwiya nazo chifukwa chiyani? Kodi ife tadya zinthu zilizonse za mfumu kapena kulandira mphatso?”
-