Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 6:3-11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kenako mfumu inatembenuka nʼkuyamba kudalitsa gulu lonse la Aisiraeli. Apa nʼkuti Aisiraeli onsewo ataimirira.+ 4 Mfumuyo inati: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene ndi pakamwa pake analonjeza bambo anga Davide ndipo ndi manja ake wakwaniritsa zimene ananena zakuti, 5 ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga mʼdziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda mʼmafuko onse a Isiraeli womangako nyumba ya dzina langa kuti likhale kumeneko.+ Ndipo sindinasankhe munthu woti alamulire anthu anga Aisiraeli. 6 Koma ndasankha Yerusalemu+ kuti dzina langa likhale kumeneko ndiponso ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+ 7 Ndipo bambo anga Davide ankafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 8 Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Unkafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina langa ndipo unachita bwino kulakalaka utachita zimenezi. 9 Koma iweyo sumanga nyumbayi, mʼmalomwake mwana wamwamuna amene udzabereke* ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 10 Yehova wakwaniritsa zimene analonjeza, chifukwa ndalowa mʼmalo mwa bambo anga Davide ndipo ndakhala pampando wachifumu wa Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza.+ Komanso ndamanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli. 11 Ndipo mʼnyumbamo ndaikamo Likasa, lomwe muli pangano+ limene Yehova anapangana ndi Aisiraeli.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena