-
2 Mafumu 19:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+
20 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya, wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndamva pemphero lako+ lokhudza Senakeribu mfumu ya Asuri.+
-
-
2 Mbiri 6:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Anthu anu Aisiraeli akagonjetsedwa ndi adani awo chifukwa choti ankakuchimwirani,+ ndiyeno abwerera kwa inu nʼkutamanda dzina lanu+ mʼnyumbayi, kupemphera+ ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo,+ 25 inuyo mumve muli kumwambako+ ndipo mukhululuke tchimo la anthu anu Aisiraeli nʼkuwabwezeretsa kudziko limene munapatsa iwowo ndiponso makolo awo.+
-