-
2 Mbiri 6:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Kumwamba kukatsekeka, mvula nʼkumakanika kugwa+ chifukwa choti akhala akukuchimwirani,+ ndiyeno iwo nʼkupemphera atayangʼana malo ano, kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya machimo awo chifukwa choti mwawapatsa chilango,+ 27 inuyo mumve muli kumwambako ndipo anthu anu Aisiraeli, omwenso ndi atumiki anu, muwakhululukire machimo awo popeza mudzawaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo.+ Mubweretse mvula+ mʼdziko lanu limene munapatsa anthu anu monga cholowa.
-