-
2 Mbiri 14:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndiyeno Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake+ kuti: “Inu Yehova, zilibe kanthu kuti anthu amene mukufuna kuwathandizawo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera mʼdzina lanu kudzamenyana ndi chigulu cha anthuchi.+ Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+
-
-
2 Mbiri 20:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako Yehosafati anaimirira pamaso pa gulu la anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, mʼnyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 nʼkunena kuti:
“Inu Yehova Mulungu wa makolo athu, kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Mʼdzanja lanu muli mphamvu ndipo palibe amene angalimbane nanu.+
-