-
Nehemiya 2:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndiyeno ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, lolani kuti ndipatsidwe makalata okasonyeza kwa abwanamkubwa a tsidya lina la Mtsinje,*+ kuti akandilole kudutsa mpaka ndikafike ku Yuda. 8 Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyangʼanira Nkhalango ya Mfumu, kuti akandipatse mitengo yokakonzera mageti a Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ yakukachisi, mpanda wa mzindawo+ ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo+ chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+
-