-
1 Mafumu 21:19-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi wapha munthu+ nʼkutenganso munda wake?”’+ Ukamuuzenso kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pamalo amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo omwewo agalu adzanyambitanso magazi ako.”’”+
20 Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. Mulungu wanena kuti, ‘Chifukwa watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+ 21 ndikubweretsera tsoka ndipo ndidzaseseratu nyumba yako ndi kupha mwamuna* aliyense wa mʼbanja la Ahabu,+ ngakhalenso ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli.+ 22 Komanso ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa ndiponso wachititsa kuti Aisiraeli achimwe.’ 23 Komanso ponena za Yezebeli, Yehova wanena kuti, ‘Agalu adzamudya Yezebeli mʼmunda wa ku Yezereeli.+ 24 Munthu aliyense wa mʼbanja la Ahabu wofera mumzinda, agalu adzamudya ndipo wofera kutchire, mbalame zidzamudya.+
-