6 Koma iwo anati: “Sitingamwe vinyo, chifukwa Yehonadabu*+ mwana wa Rekabu, kholo lathu, anatilamula kuti, ‘Inuyo kapena ana anu musamamwe vinyo mpaka kalekale.
19 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sipadzalephera kukhala munthu wa mʼbanja la Yehonadabu* mwana wa Rekabu woti azitumikira pamaso panga nthawi zonse.”’”