-
2 Mbiri 1:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndiyeno Mulungu anauza Solomo kuti: “Chifukwa zimenezi ndi zimene mtima wako ukulakalaka, ndipo sunapemphe katundu, chuma, ulemu kapenanso moyo wa anthu amene amadana nawe, sunapemphenso kuti ukhale ndi moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luso lodziwa zinthu kuti uziweruza anthu anga amene ndakupatsa kuti ukhale mfumu yawo,+ 12 ndikupatsa nzeru ndi luso lodziwa zinthu. Ndikupatsanso katundu, chuma ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhaleko ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+
-