-
1 Mafumu 1:38-40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Kenako wansembe Zadoki, mneneri Natani, Benaya+ mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti+ anapita kukakweza Solomo panyulu ya Mfumu Davide+ nʼkupita naye ku Gihoni.+ 39 Ndiyeno wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta+ mutenti+ nʼkudzoza Solomo.+ Zitatero anthuwo anayamba kuliza lipenga nʼkumafuula kuti: “Mfumu Solomo akhale ndi moyo wautali!” 40 Atatero anthuwo anayamba kumulondola ndipo ankaimba zitoliro akusangalala kwambiri, moti nthaka inangʼambika chifukwa cha phokoso lawo.+
-