24 Patapita nthawi, mkaziyo anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina lakuti Samisoni.+ Pamene mnyamatayo ankakula, Yehova anapitiriza kumudalitsa. 25 Kenako mzimu wa Yehova unayamba kumupatsa mphamvu+ ku Mahane-dani+ pakati pa Zora ndi Esitaoli.+