10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, mpaka Silo* atabwera.+ Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+
10 Awa ndi amene anali atsogoleri a asilikali amphamvu a Davide amene anamuthandiza kwambiri kulimbitsa ufumu wake pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu mogwirizana ndi mawu a Yehova okhudza Aisiraeli.+