-
2 Samueli 6:3-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma iwo ananyamulira Likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo, ana aamuna a Abinadabu, ndi amene ankatsogolera ngolo yatsopanoyo.
4 Choncho ananyamula Likasa la Mulungu woona kuchokera kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri ndipo Ahiyo ankayenda patsogolo pa Likasa. 5 Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankasangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Ankaimbanso zeze, zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana. 6 Koma atafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, Uza anagwira Likasa la Mulungu woona,+ chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa. 7 Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo Mulungu woona anamuphera+ pomwepo chifukwa chochita zinthu mopanda ulemu.+ Moti Uza anafera pompo, pafupi ndi Likasa la Mulungu woona. 8 Koma Davide anakwiya* chifukwa Yehova anakwiyira kwambiri Uza. Malo amenewa amadziwika ndi dzina lakuti Perezi-uza* mpaka lero.
-