-
2 Samueli 6:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Choncho Davide anachita mantha kwambiri ndi Yehova+ tsiku limenelo, ndipo anati: “Kodi Likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10 Davide sanafunenso kutenga Likasa la Yehova kupita nalo kumene ankakhala, ku Mzinda wa Davide.+ Mʼmalomwake Davide analamula kuti lipite kunyumba ya Obedi-edomu+ wa ku Gati.*
11 Likasa la Yehova linakhala kunyumba ya Obedi-edomu wa ku Gati kwa miyezi itatu, ndipo Yehova ankadalitsa Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+
-