-
2 Samueli 5:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Davide atachoka ku Heburoni nʼkupita ku Yerusalemu anakwatiranso akazi ena komanso anali ndi akazi apambali+ ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.+ 14 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samuwa, Sobabu, Natani,+ Solomo,+ 15 Ibara, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16 Elisama, Eliyada ndi Elifeleti.
-