15 Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, anasonkhananso pamodzi.+ 16 Choncho Hadadezeri+ anatuma anthu kuti akatenge Asiriya amene anali mʼdera la ku Mtsinje.+ Atatero anabwera ku Helamu ndipo Sobaki mkulu wa asilikali a Hadadezeri ndi amene ankawatsogolera.