-
2 Samueli 12:30, 31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Kenako anatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu* ndipo anthu anaveka Davide chipewacho. Kulemera kwake kunali kofanana ndi talente imodzi* ya golide, ndi miyala yamtengo wapatali. Iye anatenganso zinthu zambirimbiri+ mumzindawo.+ 31 Davide anatenga anthu amene anali mumzindawo nʼkuyamba kuwagwiritsa ntchito yocheka miyala, youmba njerwa komanso ntchito zina zogwiritsa ntchito zitsulo zakuthwa ndi nkhwangwa zachitsulo. Zimenezi ndi zimene anachitira anthu onse amʼmizinda ya Aamoni. Kenako Davide ndi asilikali onse anabwerera ku Yerusalemu.
-