-
2 Samueli 24:10-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Koma Davide atawerenga anthuwo, anayamba kuvutika mumtima mwake.*+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimenezi. Chonde Yehova, ndikhululukireni tchimo langa ine mtumiki wanu,+ chifukwa ndachita zopusa kwambiri.”+ 11 Davide atadzuka mʼmawa, Yehova anauza mneneri Gadi,+ wamasomphenya wa Davide, kuti: 12 “Pita, ukamuuze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali zilango zitatu zimene ndingakupatse ndipo iwe usankhepo chimodzi.”’”+ 13 Choncho Gadi anapita kwa Davide nʼkumuuza kuti: “Kodi mʼdziko lanu mugwe njala zaka 7?+ Kapena muzithawa adani anu kwa miyezi itatu?+ Kapena mʼdziko lanu mugwe mliri masiku atatu?+ Ganizirani mofatsa zoti ndikayankhe kwa amene wandituma.” 14 Davide atamva zimenezo, anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisowetsa mtendere kwambiri. Kuli bwino ndilangidwe ndi Yehova,+ chifukwa chifundo chake nʼchachikulu,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+
-