-
2 Samueli 24:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli kuyambira mʼmawa mpaka nthawi yomwe anakonza, moti anthu 70,000 anafa,+ kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ 16 Mngelo atatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha mliriwo,+ choncho anauza mngelo amene ankapha anthuyo kuti: “Basi! Bweza dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehovayo anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ wa Chiyebusi.+
-