6 Ndiyeno mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene ankakhala kumeneko. Ayebusi anayamba kunyoza Davide kuti: “Sudzalowa mumzinda uno, chifukwa ngakhale anthu osaona ndi olumala adzakuthamangitsa.” Iwo ankaganiza kuti: ‘Davide sadzalowa mumzinda muno.’+