-
2 Samueli 24:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Koma mfumu inauza Arauna kuti: “Ayi, ndikuyenera kugula zimenezi. Sindingapereke nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanga popanda kulipira chilichonse.” Choncho Davide anagula malo opunthira mbewu ndi ngʼombe ndipo analipira ndalama zokwana masekeli* 50 asiliva.+ 25 Zitatero, Davide anamangira Yehova guwa lansembe+ pamalowo ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano. Choncho Yehova anamva kuchonderera kwawo,+ moti mliri umene unagwa mu Isiraeliwo, unatha.
-