-
Numeri 31:50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
50 Choncho tiloleni kuti aliyense wa ife apereke zinthu zimene wabwera nazo monga chopereka kwa Yehova. Tabwera ndi zinthu zagolide, matcheni ovala mʼmiyendo, zibangili, mphete zachifumu, ndolo ndi zodzikongoletsera zina. Tipereka zimenezi kwa Yehova kuti ziphimbe machimo athu.”
-
-
1 Mbiri 18:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 nthawi yomweyo anatumiza mwana wake Hadoramu kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndiponso kukamuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri nʼkumugonjetsa. (Chifukwa Hadadezeri ankakonda kumenyana ndi Toi.) Popita kwa Davide, Hadoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zakopa. 11 Mfumu Davide anapereka zinthu zimenezi kwa Yehova+ pamodzi ndi siliva komanso golide amene anatenga kuchokera ku mitundu yonse. Anatenga kuchokera kwa Aedomu, Amowabu, Aamoni,+ Afilisiti+ ndi Aamaleki.+
-