-
Ekisodo 18:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli monse kuti akhale atsogoleri a anthu. Anasankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.
-
-
1 Samueli 8:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iye anawauza kuti: “Munthu amene adzakhale mfumu yanuyo azidzachita izi:+ Azidzatenga ana anu+ kuti azikayenda mʼmagaleta ake+ ndiponso kukwera pamahatchi* ake.+ Ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake. 12 Adzaika anthu ena kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake,+ kukolola mbewu zake+ ndiponso kupanga zida zake zankhondo ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+
-