-
2 Mbiri 26:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Komanso Uziya anamanga nsanja+ ku Yerusalemu pafupi ndi Geti la Pakona,+ Geti la Kuchigwa+ ndiponso pafupi ndi Mchirikizo wa Khoma ndipo nsanjazo anazilimbitsa. 10 Iye anamanganso nsanja+ mʼchipululu ndipo anakumba* zitsime zambiri (popeza anali ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela ndi kudera lafulati. Anali ndi alimi komanso anthu osamalira minda ya mpesa kumapiri ndi ku Karimeli poti iye ankakonda ulimi.
-