-
1 Mbiri 3:1-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ana amene Davide anabereka ku Heburoni+ anali awa: woyamba Aminoni,+ mayi ake anali Ahinowamu+ a ku Yezereeli, wachiwiri Danieli, mayi ake anali Abigayeli+ a ku Karimeli, 2 wachitatu Abisalomu,+ mayi ake anali Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wa 4 Adoniya,+ mayi ake anali Hagiti, 3 wa 5 Sefatiya, mayi ake anali Abitali, wa 6 Itireamu, mayi ake anali Egila mkazi wa Davide. 4 Davide anabereka ana 6 amenewa ku Heburoni ndipo analamulira kumeneko zaka 7 ndi miyezi 6. Kenako analamulira zaka 33 ku Yerusalemu.+
5 Ku Yerusalemu+ iye anabereka ana awa: Simeya, Sobabu, Natani+ ndi Solomo.+ Ana 4 amenewa mayi awo anali Bati-seba+ mwana wa Amiyeli. 6 Analinso ndi ana ena 9 awa: Ibara, Elisama, Elifeleti, 7 Noga, Nefegi, Yafiya, 8 Elisama, Eliyada ndi Elifeleti. 9 Onsewa anali ana a Davide, kuwonjezera pa ana amene akazi ake aangʼono* anamuberekera ndipo Tamara+ anali mchemwali wawo.
-