12 Komanso pamene Abisalomu ankapereka nsembe, anaitanitsa Ahitofeli+ wa ku Gilo, mlangizi wa Davide,+ kuchoka kumzinda wakwawo wa Gilo.+ Anthu amene anagwirizana ndi Abisalomu pa chiwembuchi anapitiriza kuwonjezeka.+
23 Pa nthawiyo, malangizo a Ahitofeli+ ankaonedwa ngati mawu ochokera kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu ankaonera malangizo onse a Ahitofeli.