-
1 Mafumu 13:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno anafuula mawu ochokera kwa Yehova otemberera guwalo, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa mʼnyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Iye adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akupereka nsembe yautsi pa iwe nʼkuwapereka nsembe pa iwe. Ndipo adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+
-
-
2 Mafumu 23:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Yosiya atatembenuka nʼkuona manda amene anali paphiri, anauza anthu kuti akatenge mafupa mʼmandawo ndipo anawatentha paguwa lansembelo. Anachititsa guwalo kukhala losayenera kulambirapo, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu woona uja ananena, yemwe analosera kuti zimenezi zidzachitika.+
-