-
2 Mafumu 12:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo ankapereka ndalama zimene awerengazo kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumba ya Yehova. Anthuwo ankagwiritsa ntchito ndalamazo polipira akalipentala, anthu omwe ankagwira ntchito yomanga panyumba ya Yehovayo,+ 12 amisiri omanga ndi miyala ndi anthu osema miyala. Ndalamazo anaguliranso matabwa ndi miyala yosema yokonzera nyumba ya Yehova ndiponso analipirira zonse zimene anagwiritsa ntchito pokonza nyumbayo.
-