Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:17, 18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma mtima wanu ukatembenukira kwina+ ndipo simukumvera, moti mwakopeka nʼkugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+ 18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzakhala nthawi yaitali mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu mutawoloka Yorodano.

  • Deuteronomo 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+

  • Deuteronomo 31:24-26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a Chilamulo ichi mʼbuku,+ 25 Mose analamula Alevi amene amanyamula likasa la pangano la Yehova kuti: 26 “Tengani buku ili la Chilamulo+ ndipo muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, ndipo lidzakhala mboni ya Mulungu yokutsutsani.

  • Yoswa 1:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Buku la Chilamulo ili lisachoke pakamwa pako.+ Uziliwerenga ndi kuganizira mozama* masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo.+ Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena