Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 22:14-20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Choncho wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya anapita kwa Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 15 Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Munthu amene wakutumaniyo mukamuuze kuti: 16 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake pokwaniritsa mawu onse amʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.+ 17 Chifukwa chakuti andisiya nʼkumapereka nsembe zautsi kwa milungu+ ina kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo,+ mkwiyo wanga udzayakira malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’”+ 18 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: ‘Ponena za mawu amene wamvawo, 19 chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova. 20 Nʼchifukwa chake ndidzakuika mʼmanda a makolo ako ndipo udzaikidwa mʼmanda ako mwamtendere. Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndidzabweretse pamalo ano.’”’” Kenako iwo anakauza mfumuyo zimenezi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena