-
Deuteronomo 16:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma muzidzapereka nsembe ya Pasikayo pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake. Muzidzapereka nsembeyo madzulo, dzuwa likangolowa,+ pa nthawi yofanana ndi imene munatuluka mu Iguputo. 7 Muzidzaiwotcha nʼkuidya+ pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe,+ ndipo mʼmawa mwake muzidzabwerera kumatenti anu.
-