12 Pa magulu a alonda apagetiwa, ntchito ya atsogoleri awo inali yofanana ndi ya abale awo ndipo inali yotumikira panyumba ya Yehova. 13 Choncho anachita maere+ ofanana kwa wamngʼono ndi wamkulu potsatira nyumba za makolo awo, kuti apeze ogwira ntchito pageti lililonse.